The Jaki Show

Bambo uyu, Bryan Johnson, wadzaka 47, amene tinamukambako m'mbuyomu, wasiya kudzibayira mankhwala amene wakhala akugwiritsa ntchito.

Bryan, ndi millionaire wa chuma chokwana $400 million. Iyeyu amafuna kukhala ndi moyo wamuyaya ndipo wakhala akupanga invest ma million ake kupanga mankhwala othetsa ukalamba.

Bryan wakhala akudzibaya rapamycin, mankhwala amene amagwiritsidwa ntchito kuchipatala pa operation ya transplant.

Akuti kafukufuku amene iye analipira anapeza kuti mankhwalawa, amabwezeretsa chinyamata/ chitsikana (youth).

Bryan walengeza kuti wasiya kugwiritsa ntchito mankhwalawa pamene waona kuti akupanga za opposite.

Rapamycin akumpangitsa Bryan kuoneka wamkulu kwambiri.

Sidenote

Forever young

#Nkhani #thejakishow

3 weeks ago | [YT] | 106