Talk, Vlogs, Skits


The Jaki Show

Ku USA, mayi uyu, Taylor Santiago, wa dzaka 31 wakadzipereka ku Polisi ndipo akuzengedwa mulandu.

Pa 22 January, Taylor anayitana ex-boyfriend wake kuti apite kunyumba kwake. Ex uja atapita, Taylor anamuwombera nkumupha.

Kenako Taylor anapita dela lina, kumene kunali ex-husband wake, yemwe anabelekerana naye mwana nkukamuwombera mpaka kumupha.

Anachoka pamenepo nkupita kwa ex-boyfriend wina nkumuwombera mpaka kupha. Kumeneko, anawomberanso chibwezi cha ex-boyfriend yo koma anangomuvulaza.

Atachoka pamenepo, Taylor anapita ku Polisi, kukanena zomwe wapanga nkudzipereka.

Taylor anakalowa mu court lero.

Sidenote
Chonena chikukana

#Nkhani

8 hours ago | [YT] | 33

The Jaki Show

Ku Nigeria mu mzinda wa Owerri, mayi wina wamangidwa.

Mayiyo, amene video yake ndi chithunzi chikuzungulira pa social media, anafika kunyumba kwake nkupenza wantchito wake, mtsikana wachichepere ankuonera tv ndi ana a Mayiyo.

Azi zinamuyipira mayiyo ndipo akuti anamulanga mwana wantchitoyo mpaka kupha.

Izi zadzetsa mpungwepungwe ndi mkwiyo.

Mayiyo sakutchulidwa dzina.

#Nkhani

1 day ago | [YT] | 67

The Jaki Show

A University of Oxford mogwirizana ndi ma researchers ena atatsimikiza za kupezeka kwa Super earth.

Super earth ndi planet imene inayiwona dzaka ziwiri zapitazo ndipo akhala akufufuza zambiri.

New super earth, ndiyayikulu x 6 dziko lapansi. Anayipatsa dzina lokuti HD 20794.
Akuti super earth simazungulira dzuwa lathuli koma nyenyezi ina yangati dzuwalo.

Distance yake kuchoka kwathu kuno ndi 20 light years.

Akatswiri akukhulupilira kuti uku anthu akhoza kukhalako bwinobwino nde akufufuzako.

Sidenote
20 light years mu dzaka zathu ndi 186,282 years

#Nkhani

2 days ago | [YT] | 80

The Jaki Show

Gogo wina ku China mu mzinda wa Jinxi ali ndi ma regret.
Hogo Huang Ping ali ndi nyumba ya two-storey pamalo pamene boma limafuna kumanga mseu.

Boma linamupempha Hogo kuti asamuke, anamuuza kuti amupatsa £180 000, koma Hogo anakana kuti sangasamuke.

Boma linapitiliza ma plan nkumanga mseu (motorway) kuzungulira nyumba ya Hogo.

Hogo alibe mtendere chifukwa cha magalimoto othamanga kwambiri ndi ntchito yomanga mseuyo.

Koma too late.... ndalama ija sakufuna kumupatsanso kuti asamuke.

#Nkhani

3 days ago | [YT] | 134

The Jaki Show

Ku USA, Pilot wa ndege uyu, David Allsop, wa dzaka 52, wamangidwa.

David ananyamuka, kukalowa mu ndege ali dzandidzandi ataledzera. Ndege Southwest Flight 3772, itadzadza ma passenger.

Air hostess anayitana a polisi ndipo anamunyamulamo David nkumumanga.

David akadali kundende ndipo wachotsedwa ntchito.

Side note

Komenti ikukana

#Nkhani

1 week ago | [YT] | 126

The Jaki Show

Akuti number ya anthu amene akusumila P Diddy ikufika 300.

Chabe kuti similandu yonse itakafike ku court, achita kusankha.
Pakatipa, malumewa ananyanyala ndipo anasiya kumulankhula lawyer wawo chifukwa anakanika kumutulutsista pa belo.

Pano, P Diddy akupempha kuti ma video anachotsedwa kunyumba kwake ndi a FBI atulutsidwe ndipo ayikidwe pa mbalambanda.

Iyeyu akuti ma video asonyeza kuti iye ndi osalakwa koma kuti aliyense ankapanga zomwe amafuna mosakakamizidwa.

Sidenote
Bebe oyilo dot kom

#Nkhani

2 weeks ago | [YT] | 166

The Jaki Show

Kuyambira lero, kwa ma sabata 6, ku India kuli festival ya chi Hindu yotchedwa Kumbh Mela (holy bath).

Festival imeneyi imachitika kamodzi mu dzaka 12 zilizonse.

Khamu la anthu amapita ku Sangam, mbali imene amakhulupilira kuti ndoliyodala ya mu Ganges river.

Ma Hindu amakhulupilira kuti akasamba mu ntsinje mmenemu, machimo awo amachoka ndipo mizimu yawo imatsukidwa.

Mu masiku 45 amenewa, palichiyembekezo chakuti kufika khamu la anthu okwana 400 million.

Khamuli ndilalikulu kwambiri, akuti limaoneka pa ma satellite a ku space.

#Nkhani

2 weeks ago | [YT] | 135

The Jaki Show

Bambo uyu, Bryan Johnson, wadzaka 47, amene tinamukambako m'mbuyomu, wasiya kudzibayira mankhwala amene wakhala akugwiritsa ntchito.

Bryan, ndi millionaire wa chuma chokwana $400 million. Iyeyu amafuna kukhala ndi moyo wamuyaya ndipo wakhala akupanga invest ma million ake kupanga mankhwala othetsa ukalamba.

Bryan wakhala akudzibaya rapamycin, mankhwala amene amagwiritsidwa ntchito kuchipatala pa operation ya transplant.

Akuti kafukufuku amene iye analipira anapeza kuti mankhwalawa, amabwezeretsa chinyamata/ chitsikana (youth).

Bryan walengeza kuti wasiya kugwiritsa ntchito mankhwalawa pamene waona kuti akupanga za opposite.

Rapamycin akumpangitsa Bryan kuoneka wamkulu kwambiri.

Sidenote

Forever young

#Nkhani #thejakishow

2 weeks ago | [YT] | 104

The Jaki Show

Ku USA, mtsikana uyu, Aubrey Vanlandingham, wa dzaka 17 akuzengedwa mulandu wochita nkhaza kwa zinyama.

Aubrey ali ndi mbuzi imene amayipanga train kuti idzipanga ma trick. Kumanvera ndikupanga zimene yauzidwa.

Eni mbuziwa, amalowa mipikisano ya mbuzi. Amene mbuzi yake ikuchita bwino, amapambana nkumalandira mphoto.

Mbuzi ya Aubrey imangolephera, pamene mbuzi ya mzake, yomwe anayipatsa dzina loti Willy the goat 🐐, imangowina.

Willy the Goat 🐐 anangopezeka atafa mwadzidzidzi. Achipatala atamuyeza, anapeza kuti Willy anadyetsedwa poison.

Atayang'ana ma CCTV, anawona Aubrey atalowa mu khola la Mbuziyo nkuibayira injection mkamwa.

Anayang'ana search history ya phone ya Aubrey, anapeza kuti amafusa gugo kuti pakufunika poison kwambiri bwanji kuti uphe chinyama.

Aubrey wavomera mulanduwu.

Sidenote
🐐

#Nkhani

2 weeks ago | [YT] | 82

The Jaki Show

Mhuu
Mayi uyu, ndi Erin Strotman. Ndi nurse wadzaka 26.

Amagwira ntchito ku ICU (Intensive care Unit) yosamala ana obadwa nthawi isanakwane (pre-mature).

Erin wamangidwa chifukwa chopanga nkhaza kwa makanda ongobadwa kumenewa

Akuti mpaka wathyola Mafupa a ana atatu ndipo pali chikhulupiliro chokuti anavulazanso ana ena.

Erin ali kundende kuyembekezera milandu.

Sidenote
Tingoti mphwake wa santana

#Nkhani

3 weeks ago | [YT] | 117